madah khauya tidzaonana şarkı sözleri
Nthawi yosekelera
Nthawi yokamba nthabwala
Tonse titatambalala
Yapita
Tikuona ngati kutulo
Sitidzasekanso ndi inu
Nthawi yofunsana mafunso
Kuchita kuyankha mwa luso
Pena kukanika kuyankha
Yapita
Tikuona ngati kutulo
Sitidzalankhulananso ndi inu
Nthawi yopempha yodyera
Tikamapita kusukulu
Mukatipatsa ife chimwemwe
Yapita
Tikuona ngati kutulo
Adzatipatsenso ndi ndani
Nthawi yoyankhula pa lamya
Pobwera muguleko ndiwo
Kodi mubwera liti mwasowa
Yapita oh ooh
Moyo unali okoma
Nthawi yowawa imabweleranji
Ohhhh
Gonani bwino
Ngati nkotheka
Ngati mwayi ulipo
Tidzaonana
Gonani bwino
Ngati nkotheka
Ngati mwayi ulipo
Tidzaonana
Oh ohh
Kukhala nkumakondwera
Kuti zathu zinayera
Osadziwa zidzathela
Mmasamba
Kodi imfa inakhala bwanji
Bwanji simagonjetseka
Tikudziwa ena akukondwa
Kuti mwachoka pakati pathu
Pazifukwa zodziwa okha
Chabwino oh ooh
Kusatengela zofooka
Ife tinkakukondani
Ohhh
Gonani bwino
Ngati nkotheka
Ngati mwayi ulipo
Tidzaonana
Oh oh
Gonani bwino
Ngati nkotheka
Ngati mwayi ulipo
Tidzaonana
Gonani
Tidzaonana oooooooh
Ohhh
Mesa munkanena
Zomwe mudzachite
Pamoyo wathu
Mukugonanso bwanji yeaa iiii
Mukutichokela
Munthawi yomwe
Mukufunika zedi
Pamoyo wathu oohh
Uhhh
Come on
Uuuuuuhhhhh

