t-no tribal race şarkı sözleri

Zaka zikwi zangodutsa Yesu atawonekera Mtundu wa Banthu wabadwa ufumu wake Maravi Anachokera ku Congo nkuzafikira ku nkhondo A Chewa ndi Akafula kulimbirana malowo Moto moto umabuka akamasema zitsulo Nkomwe dzina la Malawi inachokeratu ilo Anali mphepete mwa nyanja Kenako natchedwa a Nyanja Anzawo ena Amang'anja Anafika Atumbuka atadza Angonde ndi Anyakyusa anachokera ku mpoto Nkukhazikika ku Karonga kumpoto konko 1819 Angoni ndi Shaka Zulu Analimbana, Ngoni nagonja kuthawako kwa a Zulu 1840 Jumbe wafika ku Nkhotakota A Yao nagulitsa akapolo nkuwatumiza ku border Inkosi Mbelwa nkunzagonjetsa Chikulamayembe Angoni nalamula Atumbuka iwo mphavu alibe 1861, David Livingstone wafika Kuzathetsa ukapolo ndi ma mission atayambika Anayesetsa kuyankhulitsana ndi Jumbe, zinakanika Ukapolo udapitilirabe a Yao adalimbika 1870 a Yao ambiri adatsata Chisilamu Chifukwa chotengeka ndi anzawo ogulitsa akapolo Ma Scottish missionary adafika Blantyre 1876 Nkukopa akapolo amene amatengedwa ndi Apwitikizi Anayambapo kulalikira ndi kuphunzitsa muchi Nyanja Kuti afikire ambiri popeza chinatchuka ndi chi Nyanja A Tumbuka anachilandira chiphunzitso cha ma missionary mwansanga Nawo ma missionary anayamba kuphunzitsa muchitumbuka A Tonga ndi a Tumbuka anapulumuka kwa Angoni Ataphunzira kwa ma missionary napeza nzeru zoposa Ngoni 1891 British protectorate inakhazikisidwa Kugulitsa akapolo kunja kunathetsedwa 1893 ikungotukukano skulu 1895 kunatulukira a Nguru Anali mtundu wodabwitsa kuchokera ku Mozambique Analolera kugwira ntchito kwa Nzungu opanda ndalama zambiri 1904 a tsamunda anabweretsa thangata A Mang'anja, Nguru, a Sena ndi a Lomwe anagwira njakata Analima malo ambiri, kupatsidwa malo ochepa Anagwira ntchito kwambiri Koma olemera ali ena 1915 Chilembwe anawukira Nayimilira nkuwatsogoza anthu osasangalatsidwa Adagonja, tsamunda atabwenza moto naye nkulusa Anthu ambiri anaphedwa anathana ndi aliyense wotsutsa 1918 a Malawi amafuna chiyankhulo chimodzi A govenor anakana chifukwa amadana ndi umodzi A Tonga anagwirizana nkugwira zochititsa kaso A Tumbuka ndi a Ngoni, nawonso anawukanso 1933 Livingstonia inakana chi Nyanja Angoni nawo anachikana amati sichimawayanja Chitumbuka chinasanduka chiyankhulo chovomelezeka Pamodzi ndi chi Nyanja, ziwirizi zinavomelezedwa 1943 dzina la Anguru inafufutidwa Analisintha, nkuyika Lomwe ponse pomwe limatchulidwa Akachenjede odana ndi atsamunda anabwera pamodzi 1944 anagwirizana anapanga chipani chimodzi 1958 Kamuzu Banda anabwelera Nawina support ya anthu ndi MCP atayimenyelera 1964, Federation inagwa Nyasaland idapeza ufulu wodzilamulira yokha A Malawi okha okha adakangana mu cabinet crisis Kuwonetsa kuti panali ntchitobe nkatinkati mwachpanichi Chitumbuka anachiletsa, chichewa kuvomeleza Mpamene udani udapitilira nankera osalekeza It's a race that we started Tribalism is building a wall We were one race united But our difference divided us all It's a race that we started Tribalism is building a wall Nkhondo, nkhondo Kusiyanasiyanatuku kwayambitsa mpikisano
Sanatçı: T-No
Türü: Belirtilmemiş
Ajans/Yapımcı: Belirtilmemiş
Şarkı Süresi: 4:09
Toplam: kayıtlı şarkı sözü
T-No hakkında bilgi girilmemiş.

Fotoğrafı